NATIONAL NEWSNKHANI

Ophuzira akale apa sukulu ya Salima athandiza chipatala cha Salima ndizipangizo zosiyanasiyana polimbana ndi covid19

Ogwira ntchito ayamikira thandizoli

Ophunzira akale pasukulu ya secondary  ya Salima yomwe kale imkatchedwa (Salima Boys secondary), apeleka katundu wandalama wandalama zokwana 4.2 million kwacha ku chipatala cha Salima ngati njira imodzi yothandizila kuthana ndi nthenda ya covid19.

Poyankhula pamwambo opeleka katunduyu, wachiwiri kwa wapampando wa ophunzira akalewa, Enoch Phale wati anachiona chinthu chofunikira kwambili kugula kutunduyu.

“Tidakhalilana pansi ife ngati ophuzira akale apa sukulu ya sekondale ya Salima yomwe imkatchedwa Salima Boys sekondale sukulu, kutsatira uthenga wa mtsogoleri wadziko lino atalengeza kuti anthu tikuyenera titengepo gawo pothandiza momwe tingakwanitsile polimbana ndi mulili wa covid19 ndipo ngati mbali imodzi yova pempho lake komanso kupulumutsa miyoyo mchifukwa chake tagula katunduyi”.

M’mau ake mmodzi mwa akulu akulu pa chipatalachi Dr. George Kasondo wati thandizoli lafika munthawi yake.

“Thandizo limeneri ndilapamwamba kwambili ndipo lafika munthawi yake chipatala chino cha Salima chikusowekera zipangizo zambili zothandizira ogwira ntchito pachipatala chino zomwe zina ndizomwe atithandiza lelozi ndipo ndife osangalala tonse ogwira ntchito pano”.

Katundu yemwe ophuzira akalewa apeleka ndimonga zipangizo zothandira makina othandizira kupuma (Oxygen Cylinder), zovala zotchinga kukamwa ndi mphuno, zovala zotchinga kunkhope za galasi, sopo osambira m’manja mwazina.

 

Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close