NKHANI

CHIGANIZO CHA BUNGWE LA OYIMBIRA MASEWERO A MPIRA WAMIYENDO CHADABWITSA ANTHU

Bungwe la oyimbira Masewero ampira wamiyendo dziko lino la National Referees ladabwitsa anthu pomwe laika nawo oyimbira Mike Mwambyale pandanda wa anthu omwe ayimbire masewero a TNM Super League apakati pa Red Lions komanso Chitipa United kumathero a sabatayi.
Izi zikuza pomwe oyimbirayi analephera kugwira ntchito yotamandika pamasewero a league apakati pa Mighty Tigers komanso Mighty Mukuru Wanderers masabata angapo apitawa.
Pamasewerowa Mwambyale analephera kuona zina zolakwika zomwe zinachitika zomwenso zinatengera bungwe la oyimbira kulowelerapo popereka khadi yofiira kwa Christopher Kumwembe ponena kuti ndiyemwe amayenera kupasidwa chilango ngakhale oyimbirayi analephera kuona zoona zake.
Zomwe zikudabwitsa ndizoti m’malo moti oyimbirayi apasidwe chilango bungweli lapereka masewero kwa oyimbirayi yemwe azagwire ntchito pamodzi ndi Shaibu Cassim, Lesley Kuchilunda, Mphatso Mmatete komanso Chalvin Ngolanga.
M’chaka cha 2021 oyimbira Bernadettar Mkwimbira komanso Gift Chicco anapasidwa chilango atalephera kugwira bwino ntchito yawo pamasewero a Blantyre Derby omwe matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers adakumana pabwalo Kamuzu mudzinda wa Blantyre.
Izinso zikuza pomwe bungwe loyendetsa ligi yayikulu dziko lino la Super league of Malawi (Sulom) silikugona tulo pofuna kuti masewerowa apite chitsogolo.
Source ; Timveni.
Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close