NKHANI

Ayuba James atsutsa zoti akuyimira anthu milandu mwa ulele m’boma la nkhotakota.

 

Wolemba Innocent Chunga.

M’modzi mwa woyimira anthu pa milandu,yemwe ndiodziwika bwino komaso ndiyemwe adzayimire nawo pa zisakho za aphungu akunyumba ya malamulo kudera lapakati m’boma la Nkhotakota a Sylvester Ayuba James,watsutsa malipoti omwe akumveka kuti iye tsopano akuyimira anthu pamilandu m’bomali mwaulele ngati njira imodzi yochitira kampeni yake.

Polakhula ndi wayilesi ino,a James ati mphekesera yomwe ikumvekayi ndiyabodza,ponena kuti ntchito yi ndi yomwe imawapezetsa chuma,ndipo ngati anthu awafuna amawapatsa ndalama osati zomwe anthu akulakhula.

“Ndikutsimikizireni kuti ndidzapikisana nawo mu 2025 ndipo ndikawina,anthu asapange nkhani zongopeka chifukwa kuyimira milandu anthu ndi ntchito yanga yomwe imandibweletsera chuma,anthu akandifuna kuti ndikawayimile amandipatsa ndalama.Pali zinthu zochuluka zomwe zikufunika kukonzedwa kudera la kwanthu zomwe zikudikira ine,” adatero a James.

A James akuyembekezeka kudzayimira ngati phungu waku nyumba ya malamulo ouima payekha m’dera lapakati m’bomali m’zisakho za m’chaka cha 2025.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close