NKHANI

Boma likuyenera kuwonjezera ndalama ku ntchito za m’mera mpoyamba – Akatswiri.

Pamene boma pamodzi ndi mabungwe wosiyanasiyana ali pakalikiliki wolimbikitsa ntchito za m’mera mpoyamba mdziko muno,akatswiri ena amene amatsata bwino ntchitoyi ,ati boma likuyenera kuchilimika powonjenzera nthandizo lopititsira ntchito za m’mera mpoyamba patsogolo maka maka pakati pa ana obvutikitsitsa kwambiri.

Malinga ndi akatswiriwa ati angakhale kuti ndi zosabisa kuti sukulu za m’mera mpoyamba zikupeleka mwayi kwa ana obvutikitsitsa kupeza maphunziro owakonzekeletsa m’sukulu za pulaimale,iwo ati chiwerengero cha ana amene akusowekera mwayi wotere chikuchulukilabe zomweso zikusonyezelatu kuti chinthandizo ku ntchitoyi chikuyenera kukhala chambiri.

“Mukawonetsetsa zomwe zikuchitika m’madera wochulukilapo ndizakuti ana ambiri amene akusowekela mwayi watenga nawo mbali pa maphunziro a sukulu za m’mera mpoyamba ndi obvutikitsitsa. Ena mwa iwo amakhala kuti alibe pogwira,kapena ali ndi bvuto la ulumali,mwinaso nkutheka kuti akukhudzidwa ndi kachirombo komwe kamayambitsa matenda a edzi.Boma komaso ife amabungwe kumpatikizilapo mafumu ndi adindo wonse tikuyenera kuyikapo mtima ndi chidwi pa ntchito za m’mera mpoyamba,chifukwa chakuti ili ndi tsogolo la dziko,”a Moses Devlin Buscher,mkulu wa bungwe la center for children affairs Malawi,ku Chikwawa adatero.

Koma akatswiri ati boma komaso mabungwe sakuyenera kugona tulo mwezi uno wa okotobala  chifukwa chakuti ndi nthawi yabwino yomwe angaigwiritse ntchito kudziwitsa anthu komaso mabungwe wosiyanasiyana za mene ntchitoyi za m’mera mpoyamba ikuyendera mdziko muno komaso ndi ubwino wake.

A Buscher ati kuwunikidwaso kwa malamulo woyendetsera ntchito za m’mera mpoyamba mdziko muno,kunthandizira kwambiri kupititsa ntchitoyi chitsogolo,maka maka pakati pa ana obvutikitsitsa.

“Mwazina lamulo lakayendetsedwe ka ntchitoyi lawunikaso bwino chisamaliro cha alezi,amene amakhala ali ndi ana anthu tsiku lonse,komaso likupeleka mphavu zakuti ana onse zintha kumphuzilira limodzi posatengera chilema komaso nkhungu

“Tikuthokonza chifukwa chovomekeza kuwunikidwaso kwa lamuloli izi zatipatsa mangolomera kuti sitilitonkha pantchitoyi,komabe boma likuyenera kupitiliza ndi kuwonjenzera nthandizo lake kaamba koti munda wakulu koma antchito ndi wochepa

Ndipo katswiri wina a Ruth Kawale omwe amayang’anira ntchito za maphunziro ku bungwe la Save the children agwirizana ndizomwe a Buscher afotokonza potsimikiza kuti kafukufuku akusonyeza kuti kusowekela kwa nthandizo la za chuma komaso upangili pakati pa sukulu za m’mera mpoyamba mdziko muno ndi bvuto lalikulu lomwe likubwezeletsa ntchitoyi mbuyo.

“Mwachitsanzo m’sukulu zina alezi salipidwa kali konse,komaso kusowekela kwa maphunziro apadera owonjezeletsa kagwilidwe bwino ka ntchito ya alezi kumankhala ngati kumasowekelapo.Mwazina tinganene kuti ana ambiri akumaphunzira malo osasamalidwa bwino bwino woti ankhonza kubweretsa chiwopyezo pa mayo wawo,komaso kuchepa kwa zipangizo zomphunzitsira,a Kawale adatero.

Iwo adati chomwe boma lingachite ndikuyesetsa kupitiliza kuyika chidwi chake potukula ndikulimbikitsa ntchito za m’mera mpoyamba,chifukwa chakuti kupanda kulimbikitsa ntchitoyi tingathe kuyika tsogolo la ana anthu komaso dziko pachiwopysezo.

Mkulu woyang’anira ntchito za bungwe la Kindle orphan outreach ku Salima Joseph Kandiyesa nawo anatsimikiza kuti boma ndi mabungwe komaso anthu onse ndi adindo akuyenera kugwirana manja popeleka nthandizo ndi upangili woyenerera pa ntchito yolimbikitsa m’mamphunziro a sukulu za m’mera mpoyamba.

“Angakhale kuti zaka zingapo zapitazi kufikila pano nthandizo kuchokera ku boma,komaso komiti yomwe yimayang’anira ntchito za m’mera mpoyamba kunyumba ya malamulo ndi ku mabungwe wosiyana siyana lakhala likubwera,zambiri zikadatha kuchitika ndikukwanilitsidwa zopititsira ntchitoyi patsogolo kudakakhala kuti nthandizo limabwera molingana ndi ndondomeko ya zachuma choyendetsera ntchitoyi,”a Kandiyesa adatero.

Ntchito za sukulu za m’mera mpoyamba ndi njira imodzi mwandondomeko zomwe zimalimbikitsa kupeleka chisamaliro chabwino komaso choyenerera pakati pa ana,maka maka m’madera a mamphunziro,ukhondo,kadyedwe kabwino komaso kulimbitsa nthupi ndi zina zambiri.

Angakhale kuti ntchitoyi mdziko muno idayamba m’chaka cha 1950,adindo komaso anthu ambiri satengapo gawo lambiri lonthandiza boma komaso mabungwe popititsa ntchitoyi chitsogolo zomwe akatswiri ambiri omwe amatsata bwino nkhani za m’mera mpoyamba ati nthawi yakwana tsopano yakuti Malawi adzuke ndikuyamba kutengapo gawo lalikulu pa chisamaliro cha tsogolo la ana anthu.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close