NKHANI

Bungwe la FPAM aliyamikira polimbikitsa ntchito za kulera pakati achinyamata ku Salima.

Bungwe la family planning association of malawi (fpam) lomwe limalimbikitsa nkhani zakulela  lati ndilokhutila ndi mene achinyamata akulandilira ndi kutengenawopo gawo  pa tchito  ya umoyo wa bwino pakati pawo yomwe pakadalipano ikugwilidwa m’maboma asanu mdziko muno.

Mkulu woyang’anira ntchitoyi ku Salima,Frolence Mshali wati ntchitoyi ikuyang’ana kwambiri pa achinyamata powapatsa uphungu komanso zithandizo za uchembere wabwino maka kwa anthu omwe akupindula ku ntchito ya mtukula pakhomo.

“Achinyamata ambiri akumapanga zinthu mosadziwa komaso mwachibwana,makamaka akakhala kuti ali pa ubwenzi zomwe ndizopeleka chiwopysezo pa moyo ndi tsogolo lawo” Mshali adatero

Mau ake mkhalapampando wa khosolo ya Salima Ester Soko wayamikira bungwe la Fpam komaso mabungwe ena amene akulimbikitsa ntchito ya umoyo wa bwino pakati pa anyamata boma la Salima.

Malinga ndi Soko nkhani ya zakulela ndiyofunikira kwambiri popititsa ntchito za chitukuko mdziko muno

“Timakamba nthawi zambiri kuti achinyamata ndi atsogoleri a mawa,ndi chifukwa chake ntchitoyi ili yofunikira pakati pawo kuti azintha kudziwa chabwino ndi choyipa makamaka popewa kuttenga matenda ndi mimba zosakozekera” Soko adatero.

Ntchitoyi ikugwilidwa ndi thandizo lochokera ku bungwe la unicef ndipo ili m’maboma a Salima ,Balaka, Mzimba ,Dedza komanso Mangochi.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close