NKHANI

Bungwe la Habitat lachilimika ponthana ndi ulova pakati pa achinyamata boma la Salima.

Khosolo ya Salima yayamikira ntchito zomwe bungwe la Habitat ikugwira bomali ,makamaka potukula miyoyo ndi chisamaliro pakati pa achinyamata.

Mkulu woyang’anira dogosolo la kayendetsedwe ka ntchito zosiyanasiyana pa khosoloyi Moses Kaufulu ndiye wanena izi lolemba pamene bungwe la Habitat limatsegulira sukulu yomphuzitsilapo komaso kusula luso la ntchito zamanja pakati pa achinyamata kwa mfumu yayikulu Kalonga.

Malinga ndi a Kaufulu ati ali ndi chikhulupiliro kuti achinyamata ambiri apindula ndu upangili omwe adziwupeza pa sukuluyi,zomwe zingathandizile kuchepetsa bvuto la ulova pakati pa achinyamata .

“Mwachitsazo ife ngati a khosolo timakhala ndi ntchito zosiyanasiyana zachitukuko zomwe mwazina tingath kumawapatsa achinyamatawa pofuna kutukulu miyoyo yawo” adatero Kaufulu.

Potengela kuti sukuluyi yamangidwa kwa mfumu Kalonga,a Kaufulu anadandaulira bungwe la Habitat kuti liganizileso kubweretsa chitukuko chotere pakati pa mafumu ena,chifukwa chakuti achinyamata ambiri ochokera Madera atali atali sangakwanitse kufika pa sukulupa chifukwa cha bvuto la mayendedwe.

Mkulu wa bungwe la Habitat a Kelvin Kalonga wati ndi cholinga chawo kuyesetsa kuthandiza achinyamata mdziko muno kukwanilitsa zolinga zawo pomawaphuzitsa ntchito zamanja kuti adzintha kudziyimira pawokha komaso kupititsa ntchito za chitukuko m’madera mwawo.

Kalonga wati ndi chinthandizo kuchokera ku European Union (EU),bungwe la Habitat likhala likugwira ntchitoyi kwa zaka ziwiri ndi theka boma la Salima ndi ali ndi chiyembekezo pamapeto pake akhala atamphuzitsa achinyamata pwokwana 100.

“Pempho lanthu ngati bungwe la Habitat ndilakuti,tiyeni tithandizane poyang’anira chitetezo cha malowa kuti cholinga cha sukuluyi chidziwike komaso chipindulire tonse” Adatero Kalonga.

Ndipo mau ake mfumu yayikulu Kalonga yati zomwe bungwe la Habitat likuchitira anthu wokhala  m’dera lake,zobvuta kunthokoza kwake,kaamba koti kupatula kumangidwa kwa sukuluyi,bungweli lakhala likumangira nyumba anthu obvutikitsitsa kuti nawoso azigona malo abwino.

“Ndidzayesetsa pamodzi ndi adindo azanga kukhwimitsa chitetezo pa sukuluyi komaso kuwonetsetsa kuti ophuzira pa sukuluyi akhale osunga mwambo ndi cholinga chakuti loto la Habitat likwanilitsidwe pakati pa achinyamata anthu” Idafotokonza motereo gogo Kalonga.

Bungwe la Habitat likugwira ntchito zake zina ku Mulanje,Mzuzu,Blantyre,ndi Lilongwe,ndipo pakadalipano kupatula kulimbikitsa ntchito zotukulu miyoyo ndi chisamaliro cha achinyamata,bungweli lamangila nyumba anthu obvotikitsitsa okwana  pafupifupi 20,000.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close