NKHANI

Chipani cha UTM chayikira kumbuyo kukhala chete kwa m’tsogoleri wachipanichi

"Chilima wakangalika kugwira ntchito zotukula dziko, ino sinthawi yokopa anthu"

Chipani cha UTM chati utsogoleli wa chipanichi ugwilabe ntchito zake zotukula dziko osati zomwe anthu akunena pamakina mmasamba a mchezo kuti m’tsogoleli wa chipanichi a Saulos Chilima akhala chete kamba koti sakugwilizana ndizochitika zina muwutsogoleri wa boma la m’gwilizano wa Tonse.

Malingana ndi m’neneri wachpanichi, Frank Tumpale Mwenefumbo, mtsogoleri wa chipani cha UTM yemweso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Saulos Klaus Chilima wakangalika kugwira ntchito zopititsa patsogolo chitukuko chadziko lino kamba koti akukumbukira bwino kuti a Malawi adawalonjeza zochuluka.

“Ino sinthawi yopanga misonkhano yokopa anthu ayi, ndinthawi yogwira ntchito zomwe amalawi adalonjezedwa  nde m’sogoleri wathu omwe ndi a Chilima akangalika kugwira ntchito zosintha miyoyo yamalawi mogwilizana ndi mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera nde zomwe mukuti anthu akunena zakusagwilizana mu m’gwilizano wa boma la Tonse izo ndi zabodza” watero Mwenefumbo.

Kunkhani yokhudza zokozekera chisankho chapadera m’madera aphungu momwe mukuyera kuchitika chisa cha mtunduwu a Mwenefumbo ati nkhaniyi ayifotokoza moveka bwino masiku akudzawa kamba koti iwo komanso chipani cha UTM pakadali pano akulilabe anthu omwe atisiya kamba ka covid19.

“Chipani cha UTM ndichokozeka kutumikira anthu munjira zosiyanasiyana moti kubwera kwa covid19 komwe kwapangitsa kuti tiluze ena mwa aphungu athu ife zatikhudza kwambili ngati chipani moti pakadali pano tikadalira anthu omwe adatisiya koma ikadutsa nyengo imeneyi tidzakuuzani bwino lomwe ngati chipani koma pakadali pano tikulira” adawonjezera Mwenefumbo.

Covid19 mdziko muno yakhala ikutenga miyoyo ya anthu osiyanasiyana kuphatikizapo akulu akulu aboma komanso aphungu anyumba ya Malamulo zomwe zapangitsa kuti madera ena aphungu muchitikeso chisankho chapadera  tsiku lomwe silidadziwike pofuna kupeza alowa m’malo aphunguwa.

BY: Louis Khama Majamanda

Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close