MPHUNZITSI WA TIMU YA HUNGRY LIONS AYAMIKIRA BUNGWE LA FAM POYAMBITSA LIGI YA NTHANDA UNDER – 14

Wolemba Alinafe Nyanda
Mphuzitsi wa timu ya Hungry Lions wayamikira bungwe lomwe limayang’anira masewero a mpira wa miyendo m’dziko lino la Football association of Malawi (FAM),pokhazikitsa ligi ya Nthanda under -14.
Malinga ndi Kalilombe wati kubwera kwa ligi yi kunthandinzira kwambiri kusula luso achinyamata pankhani ya masewero a mpira wa miyendo.
“Ndichinthu chabwino kwambiri pakati panthu kwa imfe ngati amphunzitsi komaso osewera, ndife wothokonza ndi kubwera kwa ligi yi,zomwe tikuwona kuti zinthandinzire kwambiri kupititsa masewero a mpira wamiyendo chitsogolo,” Adatero a Kalilombe.
Kalilombe yemwe amadziwika bwino ndi kusula luso la mpira wa miyendo pakati pa achinyamata wati ali ndi chiyembekenzo kuti ligi yi itulutsa osewera ochuluka woti ankhonza kudzatumikira matimu akulu akulu.
Pakadalipano malinga ndi Kalilombe timu yake yalimbikitsa zokozekeletsa osewera kuyamba kwa ligiyi,ponena kuti ndi khumbo lawo kuti achite bwino.
Ena mwa osewera omwe adutsa manja mwa Kalilombe ndi monga wachiwiri kwa mphunzitsi wat timu ya Airborne Rangers,Asedi Ayami,katswiri wakale watimu ya Red lions Benjamin Kalua,komaso Patience Kalumo osewera wakale wa Civo ndi KB kungotchulapo wochepa chabe.