NKHANI

Kampani ya New Chigombe Ecco bricks Inthandinza mpingo wa Mpatsa CCAP kudzala mitengo boma la Salima.

Kampani ya New Chigombe Ecco bricks boma la Salima yomwe imaumba njerwa zopangidwa ndi simenti loweruka yathandinza  achinyamata ampingo wa Mpatsa CCAP kudzala mitengo m’madera wokwana asanu omwe ali pansi pa mpingowu.

Mkulu komaso mwini wake wa kampaniyi Joseph Kandiyesa wati ndi cholinga komaso khumbo la kampaniyi kutengapo gawo panothandinza boma kusamala ndi keteteza chilengedwe,pakutengera kuti njerwa zomwe kampaniyi imaumba zimanthandiziranso kusamala chilengedwe.

“lero timayakha pempho lomwe achinyamatawa adandipempha mbuyomu kuti ngati ndingawanthandinze ndi china chake choti ankhonza akuchitira mpingo pa nkhani ya chitukuko.

“Atandipempha ndinawayakhilatu pomwepo kuti chomwe ine ndingakunthandizeni ndi kukupatsani mitengo kuti mudzale,zomwe adagwilizananazo ndi chifukwa chake lero tili pano” adatero Kandiyesa.

Mtsogoleri wa achinyamata mu mpingo wa Mpatsa,Gibert Sekiteni wayamikira kampani ya New Chigombe poyakha ndi kukwanilitsa pempho lawo.

Sekiteni wati achinyamatawa ayamba ntchito yosamala ndi kuteteza chilengedwe yi molingana ndi zomwe adindo a mpingo wa khoma sinodi amfuna.

“Mpingo wanthu umayika patsogolo ntchito yosamala chilengedwe kaamba koti bvuto lakusokonekera kwa chilengedwe pa dziko lonse lapansi lakhudza aliyese nde ndi udindo wanthu ife amipingo komaso atsogoleri wosiyanasiyana kutengapo gawo” adatero Sekiteni.

Achinyamatawa adzala mitengo yokwana 2,000 ndi nthandizo lochokera ku kampani ya New Chigombe Ecco bricks,m’madera a Nakondwa,Msinda,Mkwelo,Nanyanje ndi Makande.

Mpingowu wayamikira ubale omwe ulinawo ndi Kampaniyi kaamba koti gwilizanowu unthandizira kwambiri kuti ntchito yawo yosamalira chilengedwe iyende bwino bomali.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close