NKHANI

Kusamvana pakati pa akuluakulu a chipatala cha salima ndi akuluakulu a bungwe la Waterboard mchigawo chapakati kukupeleka chiopsezo kwa anthu omwe akulandira chithandizo pachipatalachi

Wailesi ya chisomo  mogwilizana ndi bungwe la centre for human rights and rehabitation chrr yapeza kuti kusavetsetsana pakati pa akuluakulu a chipatala cha salima komanso akuluakulu a central region water board zapangitsa kuti odwala omwe akufuna kupeza thandizo pachipatachi akhale akapolo.

Bungwe la central water board anadula madzi pachipatalachi  ati pofuna kukonza ma tank koma sanafotokozere bwino kwa  akuluakulu apachipatalachi omwe pakadali pano akuloza zala akuluakuluwa kuti sanatsatile ndondomeko zabwino podula madziwakuti akonze zinazina.

potsatila polagalamu ya kwagwanji lachinayi sabata yapitachi yomwe yaulula poyera za vutoli, bungwe la CHRR lomwe limamenyela ofulu wa anthu mogwilizana ndi pologalamu ya kwagwanji ya akhakala akuchita kalondolondo wa nkhaniyi.

 

Show More

Related Articles

Leave a Reply

Back to top button
Close
Close