NKHANI

Mafco ili ndi anyamata osewera bwino mpira komaso wodzipereka watero mphuzitsi wa timuyi Stereo Gondwe.

Mphuzitsi wa timu ya Mafco Stereo Gondwe wati ndi wokhutira ndi momwe anyamata ake akuchitira,pamene asilikaliwa akukonzekera ligi ya TNM chaka chino.

Timu ya Mafco idayamba zokozekerera ligiyi sabata yantha ndipo ikuyembekezeka kubweretsa nkhope zina za tsopano pofuna kukonza pomwe padalakwika kuti atuluke mu ligi mchaka cha 2018.

Gondwe walonjenza antho wokonda timuyi kuti ayembekezere kuwonera kaseweredwe kabwino,kolimbikira komaso kopatsa chidwi kuchokera kwa asilikali aku Salima.

“Ndi Mafco yomwe ija,ambiri tilinawobe limodzi ndipo tikadalinawobe limodzi choncho sikuti ingachite kusintha kwambiri angakhale kuti mwina ndi mwina munkhonza kusintha koma zonsezi zitengera m’mene anyamata achitire

“Mafco ndi imodzi mwa ma timu omwe ali ndi anyamata osewera bwino kwambiri komaso wodzipereka ndi chifukwa chake ndikuyiwona timuyi ikuchita bwino ngati mene inkachitira mbuyomu” adatero Gondwe.

Paul khado Ndlobvu yemwe ndi mtsogoleri wa anyamata osewera mpira azake komaso amasewera kumbuyo kwa timuyi wati anthu ambiri sadayipatse mpata timuyi kuti ingathe kubwerera msanga mu ligu ya Tnm,koma zinatengera kudzikhulupilira,kusawonetsa kutopa,umodzi  ndikulimbikira.

“Unali mwezi wa disemba pomwe ndifusidwa ndi atolankhani ngati tingabwerere mwasanga mu ligi ya Tnm,ndinati komwe tikupita ku Chipiku ukuku sikwanthu sikokhalitsa tibwerelanso” adatero Ndlobvu yemwe adasakhidwanso ngati yemwe adasewera bwino kuposa azake onse mu ligi ya Chipiku mchaka cha 2019.

Koma m’modzi mwa anthu omwe amalakhulapo pa nkhani zamasewero,Thomas Shapatu Nguluwe wachenjenza Mafco kuti ikuyenera kosomekera mwanzeru anyamata ena osewera powopa kusokonenza timu.

“Ali ndi timu yabwino kwambiri zidangochitika kuti adatuluka koma anyamata amene ali ku timu imene iyi ndi abwino zedi angakhale kuti amawayang’anira pansi pa nkhani yowayitana ku timu ya dziko lino

Ngulube wati ndizosabisa kuti timu ya Mafco ikufunikira nkhope zina ngati m’meneso ma timu ambiri akuchitira chifukwa ulendo wa mchenga nkuyambira limodzi.

Iye wati ali ndi chikhulupiliro kuti Stereo Gondwe ndi omunthandizira wake Yohane Fulaye akonza timu yabwino yomwe ibwezeretse ulemerero omwe udalipo mbuyomu pakati pa anthu wokonda timuyi boma la Salima.

Masewero omwe timu ya Mafco inali nawo ndi Likumbo F.C asilikali aku Salima wa adagagada anyamata a Rashid ‘shide’Likumbo ndi zigoli zitatu kwa chimodzi pa bwalo la zamasewero la Salima.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close