NKHANI
NTHAMBI ZOMWE SIZABOMA AZIYAMIKIRA PONTHANDINZA ANTHU OMWE ADAKHUDZIDWA NDI NAMONDWE

Wolemba : Precious Kalino.
Atsogoleri akale a dziko lino Dr Bakili Muluzi ndi Dr Joyce Banda ayamikila nthambi zomwe
sizaboma kamba kamathandizo mu nthawi yake kwa anthu okhudzidwa ndi namondwe wa
Freddy.
Atsogeleri akalewa omweso ndi akazembe akufuna kwabwino kwa anthu okhudzidwa ndi
namondwe wa Freddy ayankhula izi lachisanu ku Mikolongwe Veterinary Station m’boma la
Chiradzulo pomwe amakhazikitsa ntchito yomanga nyumba zokwana 59 za anthu omwe
anakhudzidwa ndi namondweyu.
Dziko lino chaka chantha lidakhudzidwa ndi namondwe yemwe adasokonzeza mabanja ambiri komaso komaso anthu ena ambiri kutaya miyoyo yawo maka kumwera kwa dziko lino.