NKHANI
RED LIONS IWONETSA MSANA WA NJIRA KUMANGA.

Wolemba Alinafe Nyanda.
Red lions yalengenza zoti yachotsa ntchito yemwe adali mphunzitsi wa timu yi Mike Kumanga chifukwa chakupitilira kwa kusachita bwino kwa timuy yi.
Malinga ndi yemwe amalakhulira timu ya Red lions ,Peter Chitsulo,pakadalipano atsogoleri atenga yemwe adali woyang’anira amphuzitsi a timu yi Franco Ndawa kukhala wongogwilizira.
Masewero ake oyamba a Ndawa yemwe adamphuzitsako ma timu ochulukilapo m’dziko muno monga FCB Nyasa Big Bullets,Mighty Mukuru Wanderes,Mighty Tigers,Civil Service Club komaso Silver Strikers alipo la mulungu pomwe Red Lions ikuyembekezeka kusosolana nthenga ndi Chitipa Unite pa bwalo la za masewero la Balaka.
Kuchotsedwa kwa Kumanga kwadza pamene timuyi ili panambala 15 mundandanda wa matimu omwe akusewera mu TNM Super league,ndipo yakwanilitsa kutolera mapointi anayi pa masewero asanu ndi atatu yomwe yasewera pakadalipano.
Kumanga wankhala mphunzitsi wachiwiri wa matimu a chisilikali ,kuchotsedwa ntchito yake ngati mphunzitsi wa mpira wa miyendo,pakutsatira kwa kuchotsedwa kwa mphunzitsi wa timu ya Mafco Sterero Gondwe yemwe adasinthana ndi Prichard Mwanza.