NKHANI

SUKULU YA MZUNI YATSEKEDWA

Sukulu ya ukachenjede ya mzuni yatsekedwa kutsatila zionetselo zomwe zinachitika dzulo
Kamba kakusakondwa ndi kukwera kwa ndalama yolipilira maphunziro awo.

Malingana ndi kalata yomwe akuluakulu asukuluyi atulutsa ndikusaindwa ndi olembetsa pa
sukuluyi, Yonam Ngwira ophunzira onse auzidwa kuchoka pa sukuluyi lero.

Pakadali pano a police mu nzindwa wa Mzuzu kudzela kwa mneneli wawo ,Paul Tembo atsimikiza zakumangidwa kwa ophunzira okwana 16 omwe mwa iwo 11 ndi amuna ndipo asanu ndi akazi.

Tembo wati Ophunzirawa awatsekulira mlandu odzetsa chisokonezono ndipo akuembekeza
kukaonekela ku bwalo la milandu posachedwapa .

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close