NKHANI

Timu ya Silver Strikers yatsimikiza zakuyimitsidwa ntchito kwa Mtetemera.

Wolemba Noel Bauleni.

Mkulu woyendetsa zintchito za timu ya Silver Strikers,Thoko Chimbali wati Mtemera wayamba wayimitsidwa kaye ndi cholinga chofuna kuti ayambe wafufuzidwa kaye pazomwe akumuganizila.

Chimbali wati wachiwiri wina kwa mphuzitsi wa timuyi Macdonald Yobe pamodzi ndi mphuzitsi wamkulu  Denis Kabwe ankhala akupitilinza kuphuzitsa timuyi.

Koma Chimbali wakana kufotokonza zambiri zokhudzana ndikuyimitsidwa kwa Mtetemela ponena kuti kafukufuku adakali mkati.

Koma m’modzi mwa anthu omwe amalakhulapo pankhani zamasewero Kimu Kamau wati zomwe zachitika ku banja la Silver Strikers masiku awiri apitawa zingathe kusokonenza malingaliro atimuyi ofuna kutenga ligi ya TNM.

Kamau wati mwazina zomwe zikuchitika ku bankers zinkhonza kubalalitsa anyamata osewera mpira ankhale kuti timuyi idakali ndi masewero ena obvuta monga a muchikho cha fhd bank ndi timu ya Bullets yomwe ywagonjetsa posachedwapa.

Pakadalipano timu ya Silver Strikers ili pa pa number two ndi ma points wokwana 46 masewero wokwana 23 omwe yasewera mu ligi ya TNM Superleague.

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close