NKHANI

ULEMU MSUNGAMA WAKHUMUDWITSA MAFUMU KU AREA 23

Msungama wati mafumu aku area 23 ndi madeya

Wolemba : Alinafe Nyanda

Mafumu aku area 23,kwa mfumu yayikulu Tsabango boma la Lilongwe ati ndi wokhumudwa ndi mau ochokera mkamwa mwa phungu wa dela la kumwera kumawa kwa bomali a Ulemu Msungama.

Malinga ndi mafumu wa ati ndizomvetsa chisoni komaso zosapatsa ulemu kuti azinyonzeka ndikulakhulidwa ngati ana chifukwa chogwira nthito yawo mosakondera komaso moyenera.

Potsimikiza za kusakondwa ndi zomwe achita a Msungama pakati pawo,mfumu Uledi Chalera Ng’oma komaso mfumu Christine Gamaliyeli ati phungu yu adalakwitsa ponena atsogoleriwa kuti ndi madeya.

A Msungama adawunza mafumuwa kuti ndi madeya komaso anthu osadalilika chifukwa choti akulandira anthu ena omwe awonetsa chidwi chofuna kudzapikisana ndi Msungama pa mpando wa phungu wa nyumba yamalamulo

“Tangoganizani mafumu wonse pafupifupi 38 kunenedwa kuti ndi madeya kaamba koti akulandira anthu omwe akufuna kudzayesa nawo mwayi pa chisakho mchaka cha 2025. Ife ngati mafumu tikuwona kuti phunguyu adatha mtnda sadatilakhule bwino,chifukwa ife sitingakhale madeya chifukwa cholandira ana anthu amudzi omwe akufuna kudzapikisana nawo,” idatero mfumu Gamaliyele.

Ndipo mau ake mfumu Chalera Ng’oma yati nthawi zina aphungu wa azintha kumvetsetsa ndi kumvomerenza kuti mpandowu amapikisana ndi nzika iliyonse yomwe ilinkuthekera ikhonza kutenga nawo gawo mosawopsenza,ponena kuti zomwe akupanga a Msungama ndikufuna kuwopsenza mafuma.

A Msungama adalakhula izi pa mkuman omwe adali nawo ndi mafumu wa pa sukulu ya Mlodza Secondary School.

Ena mwa anthu omwe akuwonetsa chidwi chofuna kudzapikisana ndi a Msungama delali ndi monga m’modzi mwa anthu wodziwika pa ntchito za malonda ku area 23 a Mose komaso mfumu ya mzinda wa Lilongwe Richard Banda.

 

Tags
Show More

Related Articles

Back to top button
Close
Close