NKHANI
Unduna waza umoyo wati uyamba kugawa ma net woteteza ku udzudzu m’boma la Salima
Wolemba Melie Chipula Bayani.
Unduna waza umoyo wati uyamba kugawa ma net woteteza ku udzudzu m’boma la Salima mu miyezi ya October komanso November mboma li.
Poyankhula pa mkumano wa atengambali ochokela ku Mthambi zosiyanasiyana m’boma a Salima, mkulu wowona za nthenda ya malungo pa chipatala cha Salima Cosmas Phiri wati kugawidwa kwa ma net wa kwadza kaamba ka kuchuluka kwa chiwelengero cha anthu odwala nthenda ya Malungo.